Zikomo kwambiri wolemekezeka a Jinford Maulidi komanso a George Qoma potilandira m'madera mwanu ku Chikwawa west komanso Chikwawa Nkhate, pamene BEAM inazakuchezerani.
Ngati Beautify Malawi, timadziwa kuti munthu amene ali ndi njala sangathe kugwira ntchito za chitukuko ndi zopindulitsa m'dera lake ndipo pa chifukwa ichi, gawo lina la ntchito zathu ndi kuthandiza abale omwe ali wochepekedwa.
Tiyeni tonse tigwirane manja pamene tikubwenzeretsa kukongola kwa dziko lathu. Chimodzimodzinso, tonse omwe tili ndikuthekera kothandiza ena, tiyeni tifikire amzanthu ndi thandizo.